The Madonna of the Streets
Mary's Rosaries

Home Page

Contact Us

Make a Payment, Methods of Payment, Refund and Exchange Policies

Rosaries
subpages:

How to Pray the Rosary
subpages:

Pictures Main Page
subpages:

Curriculum
subpages:

Website Terms of Use

License Agreement

Sitemap


The Work of God's Children

Chichewa Rosary Prayers
This dialect is also known as Chewa, Cheva, and Sheva.
This is a dialect of Nyanja spoken in Malawi, Zambia, and Zimbabwe.

See also The Work of God's Children page for the illustrated version of prayers in this language.

The Sign of the Cross / Signum Crucis
+ M'DZINA LA ATATE NDI LA MWANA NDI LA MZIMU WOYERA, AMEN.

Kumvera kwa Apostoli  / The Apostles' Creed / Credo

Ine ndimvera Mulungu AtateAmphamvuzonse amene adalenga

zakumwamba ndi zapansi pano. Ndimveranso Yesu Khristu Mwana

wake yekha, Ambuye athu, amene adayikidwa m'mimba ndi mphamvu

za Mzimu Woyera nabadwa mwa Maria Virigo, adamsautsa kwa Ponsio

Pilato. Adampachika pamtanda, namwalira, adamuyika m'manda,

adalowa m'limbo ndipo mkucha wake adauka kwa akufa, adakwera

kumwamba nakhala padzanja lamanja la Mulungu Atate

Amphamvuzonse. Adzafumira komweko kudzaweruza amoyo ndi akufa.

Ndipo ndimvera Mzimu Woyera, Eklezia Katolika Woyera, ndimveranso

kuti Oyera ayanjana, Mulungu atikhululukira machimo, thupi lidzauka,

ulipo moyo osatha. Amen.

Another version of
CHIKHULUPILIRO CHA APOSITOLI / The Apostles' Creed / Credo

Ndikhulupilira Atate Mulungu Mlengi wakumwamba ndi dziko

lapansi. Ndi mwa Yesu Khrisitu, Mwana wake yekha, wa Atate

athu. Kudzera Mumzimu Woyera, anabadwa kwa mai Maria.

Anadzudzidwa ndi Apolinto Pilato, anakhomedwa pa mtanda,

nafa ndi kuikidwa m’manda, ndikukhala ndi akufa. Tsiku

latchitatu anauka kwa akufa. Anapita kumwamba, nakakhala

kudzanja lamanja la Mulungu Atate waphamvu zonse.

Kuchokera kumwamba adzabwera kudzaweruza amoyo ndi

akufa. Ndikhulupilira mu M’zimu Woyera. Ndikhulupilira

tchalichi cha akatolika oyera, ndichigwirizano cha angelo.

Kukhulukiridwa kwa machimo. Kuuka kwa akufa. Ndikukhala

ndi moyo wosatha. Amen.Atate Athu / Our Father / Pater Noster
Atate athu, muli mwamba,
Dzina lanu liyeretsedwe.
Ufumu wanu udze.
Kufuna kwanu kucitidwe,
Monga kumwamba choncho pansi pano.
Mutipatse lero chakudya chathu chalero.
Mutikhululukire zochimwa zathu.
Monga ifenso tikhululukira adani athu.
Musatisiye ife muchinyengo.
Koma mutipulumutse ife kwa zoyipa.
Amen.Another version of
Atate Athu / Our Father / Pater Noster

Atate athu muli m'mwamba, dzina lanu
liyeretsedwe, ufumu wanu udze, kufuna kwanu
kuchitidwe, monga kumwamba choncho pansi pano.
Mutipatse ife lero chakudya chathu cha lero.
Mutikhululukire ife zochimwa zathu monga
ifenso tiwakhululukira adani
athu, musatisiye ife m'chinyengo koma mutipulumutse ife kwa zoyipa.  Amen.
 


Tinione Maria / Hail Mary / Ave Maria
Tinione Maria,
Wachaulere chodzaza,
Ambuye ali nanu.
Ndinu wodala mwa akazi onse
Wodalanso ndi mwana wanu Yesu.
Maria oyera,
Amayi a Mulungu,
Mutipempherere ife ochimwa
Tsopano ndi panthawi yakufa kwathu.
Amen.

Another version of
Tikuoneni Maria / Hail Mary / Ave Maria
 Tikuoneni Maria wa chaulele chodzadza,
Ambuye ali nanu.
Ndinu odala mwa akazi onse,
Ngodalanso mwana wanu Yesu.
Maria oyera amayi a mulungu
mutipempherere ife,
Tsopano ndi pa nthawi zosatha.
Amen.

Another version of
Tikuoneni Maria / Hail Mary / Ave Maria
Tikuoneni Maria wa chaulere chodzaza
Ambuye ali nanu, ndinu
wodala mwa akazi onse
ndipo ngodalanso
Mwana wanu Yesu.
Maria woyera Amayi a Mulungu
mutipempherere ife ochimwa, tsopano ndiponso pa nthawi ya kufa kwathu Amen.

Malamulo a Mulungu  / The Ten Commandments

Usapembedze Mulungu wina koma ine ndekha.

Usatchule pachabe dzina la Ambuye Mulungu wako.

Udzikumbikira kuyeretsa tsiku lamulungu.

Lemekeza atate ako ndi amayi ako.

Usaphe.

Usachite chigololo.

Usabe.

Usachite umboni onama.

Usasirire ukwati wamwini.

Usachite kaduka ndi zinthu zamwini.

Ulemu Kwa Mulungu Kumwamba / Glory to God in the Highest / Gloria

Ulemu kwa Mulungu kumwamba, ndipo pansi pano

mtendere kwa anthu chifukwa iye akuwakonda.

Tikukuyamikani, tikukutamandani, Tikukupembedzani

tikukulemekezani, tikukuthokozani chifukwa cha

ulemu wanu waukulukulu. Inu Ambuye Mulungu, Mfumu wakumwamba,

Mulungu Atate a mphamvu zonse. Inunso Ambuye Yesu Khristu,

Mwana wake mmodzi yekha, Ambuye Mulungu,

Kankhosa ka Mulungu, Mwana wa Atate,

Inu amene mumachotsa machimo a anthu, mutichitire chisoni;

Inu amene mumachotsa machimo a anthu, Mverani mapemphero athu;

Inu amene mumakhala pa dzanja lamanja la Atate mutichitire chisoni.

Poti inu nokha, Yesu Khristu, ndinu woyera; Inu nokha ndinu Ambuye,

Inu no

kh

a ndinu wopambana ndithu, limodzi ndi Mzimu Woyera, mu ulemu wa Mulungu Atate.

Usikuwo woyerawo / Silent Night/Stille Nacht

Usikuwo woyerawo,
Mwana adamlerayo,
Akakhale Mfumuyo,
Adabadwa m'kholamo,
Mfumu yamafumu
Ndi ya anthuwo.

Creative Commons License
The contents of this webpage are licensed under a Creative Commons Attribution 3.0 License.
Valid HTML 4.01 Transitional
(this is the bottom of page)