Banti
Rosary Prayers
This language is a
dialect of
Mundani.
This language is spoken
by 34,000 people in the
South West Province, Manyu Division, Mamfe and northern Fontem
subdivisions, and south of Batibo in Cameroon.
See also The
Work
of God's Children page for the illustrated version of prayers
in this language.
+ The Sign of the Cross / Signum
Crucis
+ M'DZINA
LA ATATE NDI + LA MWANA NDI + LA MZIMU WOYERA, AMEN.
Kumvera
kwa Apostoli / The Apostles' Creed / Credo
Ine
ndimvera Mulungu AtateAmphamvuzonse amene adalenga
zakumwamba
ndi zapansi pano. Ndimveranso Yesu Khristu Mwana
wake
yekha, Ambuye athu, amene adayikidwa m'mimba ndi mphamvu
za
Mzimu Woyera nabadwa mwa Maria Virigo, adamsautsa kwa Ponsio
Pilato.
Adampachika pamtanda, namwalira, adamuyika m'manda,
adalowa
m'limbo ndipo mkucha wake adauka kwa akufa, adakwera
kumwamba
nakhala padzanja lamanja la Mulungu Atate
Amphamvuzonse.
Adzafumira komweko kudzaweruza amoyo ndi akufa.
Ndipo
ndimvera Mzimu Woyera, Eklezia Katolika Woyera, ndimveranso
kuti
Oyera ayanjana, Mulungu atikhululukira machimo, thupi lidzauka,
ulipo
moyo osatha. Amen.
Atate Athu /
Our Father
Atate athu, muli mwamba,
Dzina lanu liyeretsedwe.
Ufumu wanu udze.
Kufuna kwanu kucitidwe,
Monga kumwamba choncho pansi pano.
Mutipatse lero chakudya chathu chalero.
Mutikhululukire zochimwa zathu.
Monga ifenso tikhululukira adani athu.
Musatisiye ife muchinyengo.
Koma mutipulumutse ife kwa zoyipa.
Amen.
Another
version
of
Atate Athu / Our
Father / Pater Noster
Atate
athu muli m'mwamba, dzina lanu
liyeretsedwe,
ufumu wanu udze, kufuna kwanu
kuchitidwe,
monga kumwamba choncho pansi pano.
Mutipatse
ife lero chakudya chathu cha lero.
Mutikhululukire
ife zochimwa zathu monga
ifenso
tiwakhululukira adani
athu,
musatisiye ife m'chinyengo koma mutipulumutse ife
ku zoyipa. Amen.
Tinione Maria /
Hail Mary / Ave Maria
Tinione Maria,
Wachaulere chodzaza,
Ambuye ali nanu.
Ndinu wodala mwa akazi onse
Wodalanso ndi mwana wanu Yesu.
Maria oyera,
Amayi a Mulungu,
Mutipempherere ife ochimwa
Tsopano ndi panthawi yakufa kwathu.
Amen.
Another version of
Tikuoneni
Maria / Hail Mary
Tikuoneni
Maria wa chaulele chodzadza,
Ambuye ali nanu.
Ndinu odala mwa
akazi onse,
Ngodalanso mwana wanu Yesu.
Maria oyera amayi a
mulungu
mutipempherere ife,
Tsopano ndi pa nthawi zosatha.
Amen.
Another version of
Tikuoneni
Maria
/
Hail Mary / Ave Maria
Tikuoneni
Maria wa chaulere chodzaza
Ambuye
ali nanu, ndinu
wodala
mwa akazi onse
ndipo
ngodalanso
Mwana
wanu Yesu.
Maria
woyera Amayi a Mulungu
mutipempherere
ife ochimwa, tsopano ndiponso pa
nthawi ya kufa kwathu Amen.
Malamulo
a Mulungu / The Ten Commandments
Usapembedze
Mulungu
wina
koma ine ndekha.
Usatchule
pachabe
dzina
la Ambuye Mulungu wako.
Udzikumbikira
kuyeretsa
tsiku
lamulungu.
Lemekeza
atate
ako
ndi amayi ako.
Usaphe.
Usachite
chigololo.
Usabe.
Usachite
umboni
onama.
Usasirire
ukwati
wamwini.
Usachite
kaduka ndi zinthu zamwini.
Ulemu
Kwa Mulungu Kumwamba / Glory to God in the Highest / Gloria
Ulemu
kwa
Mulungu
kumwamba, ndipo pansi pano
mtendere
kwa
anthu
chifukwa iye akuwakonda.
Tikukuyamikani,
tikukutamandani,
Tikukupembedzani
tikukulemekezani,
tikukuthokozani
chifukwa
cha
ulemu
wanu
waukulukulu.
Inu Ambuye Mulungu, Mfumu wakumwamba,
Mulungu
Atate
a
mphamvu zonse. Inunso Ambuye Yesu Khristu,
Mwana
wake
mmodzi
yekha, Ambuye Mulungu,
Kankhosa
ka
Mulungu,
Mwana wa Atate,
Inu
amene mumachotsa machimo a anthu, mutichitire chisoni;
Inu
amene mumachotsa machimo a anthu, Mverani mapemphero athu;
Inu
amene mumakhala pa dzanja lamanja la Atate mutichitire chisoni.
Poti
inu
nokha,
Yesu Khristu, ndinu woyera; Inu nokha ndinu Ambuye,
Inu
nokha ndinu wopambana ndithu, limodzi ndi Mzimu Woyera, mu ulemu wa
Mulungu Atate.
|